Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 29:1-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo mwezi wacisanu ndi ciwiri, tsiku loyamba la mweziwo, muzikhala nako kusonkhana kopatulika; musamacita nchito ya masiku ena; likukhalireni inu tsiku lakuliza malipenga.

2. Pamenepo muzipereka nsembeyopsereza ya pfungo lokoma kwa Yehova; ng'ombe imodzi yamphongo, nkhosa yamphongo imodzi, ana a nkhosa asanu ndi awiri a caka cimodzi opanda cirema;

3. ndi nsembe yao yaufa, ufa wosalala wosanganiza ndi mafuta, atatu a magawo khumi akhale a ng'ombeyo, awiri a magawo khumi akhale a nkhosa yamphongo,

4. ndi limodzi la magawo khumi likhale la mwana wa nkhosa mmodzi, momwemo ndi ana a nkhosa asanu ndi awiri;

5. ndi tonde mmodzi wa nsembe yaucimo, yakutetezera inu;

6. pamodzi ndi nsembe yopsereza ya pamwezi, ndi nsembe yace yaufa, ndi nsembe yopsereza yosalekeza, ndi nsembe yace yaufa, ndi nsembe zace zothira, monga mwa lemba lace, zikhale za pfungo lokoma, nsembe yamoto ya Yehova.

7. Ndipo tsiku la khumi la mwezi wacisanu ndi ciwiri uwu muzikhala nako kusonkhana kopatulika; pamenepo mudzicepetse; musamagwira nchito;

8. koma mubwere nayo nsembe yopsereza kwa Yehova, ya pfungo lokoma; ng'ombe yamphongo imodzi, nkhosa yamphongo imodzi, ana a nkhosa asanu ndi awiri a caka cimodzi; akhale kwa inu opanda cirema;

9. ndi nsembe yao ya ufa wosalala wosanganiza ndi mafuta, atatu a magawo khumi akhale a ng'ombe, awiri a magawo khumi akhale a nkhosa yamphongo imodziyo;

10. limodzi la magawo khumi likhale la mwana wa nkhosa mmodzi, momwemo ndi ana a nkhosa asanu ndi awiri;

11. tonde mmodzi akhale nsembe yaucimo, pamodzi ndi nsembe yaucimo yotetezera, ndi nsembe yopsereza yosalekeza, ndi nsembe yace yaufa, ndi nsembe zace zothira.

12. Ndipo tsiku lakhumi ndi cisanu la mwezi wacisanu ndi ciwiri muzikhala nako kusonkhana kopatulika; musamacita nchito ya masiku ena, koma mucitire Yehova madyerero masiku asanu ndi awiri;

13. ndipo mubwere nayo nsembe yopsereza, ndiyo nsembe yamoto, ya pfungo lokoma kwa Yehova: ng'ombe zamphongo khumi ndi zitatu, nkhosa zamphongo ziwiri, ana a nkhosa khumi ndi anai, a caka cimodzi, akhale opanda cirema;

Werengani mutu wathunthu Numeri 29