Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 28:7-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. Ndi nsembe yace yothira ya mwana wa nkhosa mmodziyo ndiyo limodzi la magawo anai la bini; m'malo opatulika uthirire Yehova nsembe yothira ya cakumwa colimba.

8. Ndi mwana wa nkhosa winayo umpereke madzulo; monga nsembe yaufa ya m'mawa, ndi nsembe yothira yace, umpereke; ndiyo nsembe yamoto ya pfungo lokoma la Yehova.

9. Ndipo dzuwa la Sabata ana a nkhosa awiri a caka cimodzi, opanda cirema, ndi awiri a magawo khumi a efa wa ufa wosalala, ukhale nsembe yaufa, wosanganiza ndi mafuta, ndi nsembe yace yothira;

10. ndiyo nsembe yopsereza ya dzuwa la Sabata liri lonse, pamodzi ndi nsembe yopsereza yosalekeza, ndi nsembe yace yothira.

11. Ndipo poyamba miyezi yanu muzibwera nayo nsembe yopsereza ya Yehova: ng'ombe zamphongo ziwiri, ndi nkhosa yamphongo imodzi, ndi ana a nkhosa asanu ndi awiri a caka cimodzi opanda cirema;

Werengani mutu wathunthu Numeri 28