Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 28:2-5 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. Uza ana a Israyeli, nuti nao, Muzisamalira kubwera naco kwa Ine copereka canga, cakudya canga ca nsembe zanga zamoto, ca pfungo lokoma, pa nyengo yace yoikika.

3. Ndipo unene nao, Nsembe yamoto imene muzibwera nayo kwa Yehova ndiyi: ana a nkhosa awiri a caka cimodzi opanda cirema, tsiku ndi tsiku, nsembe yamoto yosalekeza.

4. Mwana wa nkhosa mmodziyo umpereke m'mawa, ndi mwana wa nkhosa winayo umpereke madzulo;

5. ndi limodzi la magawo khumi la efa wa ufa wosalala ukhale nsembe yaufa, wosanganiza ndi limodzi la magawo anai la bini wa mafuta opera.

Werengani mutu wathunthu Numeri 28