Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 27:5-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Ndipo Mose anapita nao mlandu wao pamaso pa Yehova.

6. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,

7. Ana akazi a Tselofekadi anena zaona; uwapatse ndithu colowa cikhale cao cao pakati pa abale a atate wao; nuwalandiritse colowa ca atate wao.

8. Ndipo unene ndi ana a Israyeli, ndi kuti, Akafa munthu wamwamuna wopanda mwana wamwamuna, colowa cace acilandire mwana wace wamkazi.

9. Ndipo akapanda kukhala naye mwana wamkazi, mupatse abale ace colowa cace.

10. Ndipo akapanda kukhala nao abale, mupatse abale a atate wace colowa cace.

11. Ndipo akapanda abale a atate wace, mupatse wa cibale cace woyandikizana naye wa pfuko lace colowa cace, likhale lace lace; ndipo likhale kwa ana a Israyeli lemba monga Yehova wamuuza Mose.

12. Ndipo Yehova anati kwa Mose, Kwera m'phiri ili la Abarimu, nupenye dziko limene ndapatsa ana a Israyeli,

13. Utaliona iwenso udzaitanidwa kumka kwa anthu a mtundu wako, monga anaitanidwa Aroni mbale wako;

14. popeza munapikisana nao mau anga m'cipululu ca Zini, potsutsana nane khamulo, osandipatula Ine pa madziwo pamaso pao. Ndiwo madzi a Meriba m'Kadesi, m'cipululu ca Zini.

15. Ndipo Mose ananena ndi Yehova, nati,

Werengani mutu wathunthu Numeri 27