18. Ndipo Yehova anati kwa Mose, Utenge Yoswa mwana wa Nuni, ndiye munthu mwa iye muli mzimu, nuike dzanja lako pa iye;
19. numuimike pamaso pa Eleazara wansembe, ndi pamaso pa khamu lonse; numlangize pamaso pao.
20. Ndipo umuikirepo ulemerero wako, kuti khamu lonse la ana a Israyeli ammvere.
21. Ndipo aime pamaso pa Eleazara wansembe, amene amfunsire monga mwa ciweruzo ca Urimu pamaso pa Yehova; ponena iye azituruka, ndi ponena iye azilowa, ndi iye ndi ana onse a Israyeli pamodzi naye, ndiwo khamu lonse.
22. Ndipo Mose anacita monga Yehova adamuuza; natenga Yoswa namuimitsa pamaso pa Eleazara wansembe, ndi pamaso pa khamu lonse;
23. namuikira manja ace, namlangiza monga Yehova adanena ndi dzanja la Mose.