Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 26:8-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Mwana wamwamuna wa Palu ndiye Eliyabu.

9. Ndi ana a Eliyabu: Nemueli, ndi Datani ndi Abiramu. Iwo ndiwo Datani ndi Abiramu omwe aja oitanidwa a khamu, amene anatsutsana ndi Mose ndi Aroni mu msonkhano wa Kora, mula anatsutsana ndi Yehova;

10. ndipo dziko linayasama pakamwa pace, ndi kuwameza pamodzi ndi Kora, pakufa msonkhano uja; muja mote unaononga amuna mazana awiri ndi makumi asanu, nakhala iwo cizindikilo.

11. Koma sanafa ana amuna a Kora.

12. Ana amuna a Simeoni monga mwa mabanja ao ndiwo: Nemueli, ndiye kholo la banja la Anemueli; Yamini, ndiye kholo la banja la Ayamini; Yakini, ndiye kholo la banja la Ayakini;

13. Zera, ndiye kholo la banja la Azera; Sauli, ndiye kholo la banja la Asauli.

14. Iwo ndiwo mabanja a Asimeoni, zikwi makumi awiri mphambu ziwirikudzamazana awiri.

15. Ana amuna a Gadi monga mwa mabanja ao ndiwo: Zefoni, ndiye kholo la banja la Azefoni; Hagi, ndiye kholo la banja la Ahagi; Suni, ndiye kholo la banja la Asuni;

16. Ozini, ndiye kholo la banja la Aozini; Eri, ndiye kholo la banja la Aeri;

17. Arodi, ndiye kholo la banja la Aarodi; Areli, ndiye kholo la banja la Aareli.

18. Iwo ndiwo mabanja a ana a Gadi, monga mwa owerengedwa ao, zikwi makumi anai ndi mazana asanu.

Werengani mutu wathunthu Numeri 26