Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 26:36-39 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

36. Ndipo mwana wamwamuna wa Sutela ndiye Erani, ndiye kholo la banja la Aerani.

37. Iwo ndiwo mabanja a ana a Efraimu monga mwa owerengedwa ao, ndiwo zikwi makumi atatu mphambu ziwiri kudza mazana asanu. Iwo ndiwo ana amuna a Yosefe monga mwa mabanja ao.

38. Ana amuna a Benjamini monga mwa mabanja ao ndiwo: Bela, ndiye kholo la banja la Abela; Asibeli, ndiye kholo la banja la Aasibeli; Ahiramu, ndiye kholo la banja la Aahiramu;

39. Sufamu ndiye kholo la banja la Asufamu; Hufamu, ndiye kholo la banja la Ahufamu.

Werengani mutu wathunthu Numeri 26