19. Ana amuna a Yuda, ndiwo Eri ndi Onani; ndipo Eri ndi Onani anamwalira m'dziko la Kanani.
20. Ndipo ana a Yuda monga mwa mabanja ao ndiwo: Sela, ndiye kholo la banja la Asela; Perezi, ndiye kholo la banja la Aperezi; Zera, ndiye kholo la banja la Azera.
21. Ndipo ana a Perezi ndiwo: Hezeroni, ndiye kholo la banja la Ahezeroni; Hamuli, ndiye kholo la banja la Ahamuli.
22. Iwo ndiwo mabanja a Yuda monga mwa owerengedwa ao, zikwi makumi asanu ndi awiri mphambu zisanu ndi cimodzi kudza mazana asanu.
23. Ana amuna a Isakara monga mwa mabanja ao ndiwo: Tola, ndiye kholo la banja la Atola; Puva, ndiye kholo la banja la Apuni;
24. Yasubi, ndiye kholo la banja la Ayasubi; Simironi, ndiye kholo la banja la Asimironi.
25. Iwo ndiwo mabanja a Isakara monga mwa owerengedwa ao; zikwi makumi asanu ndi limodzi mphambu zinai kudza mazana atatu.