Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 25:1-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Israyeli anakhala m'Sitimu, ndipo anthu anayamba kucita cigololo ndi ana akazi a Moabu;

2. popeza anaitana anthuwo adze ku nsembe za milungu yao; ndipo anthuwo anadya, nagwadira milungu yao.

3. Pamene Israyeli anaphatikana ndi Baala Peori, Mulungu anapsa mtima pa Israyeli.

4. Ndipo Yehova anati kwa Mose, Gwira akuru onse a anthu nuwapacikire Yehova, pali dzuwa poyera, kuti mkwiyo waukali wa Yehova ucoke kwa Israyeli.

5. Ndipo Mose anati kwa oweruza a Israyeli, Iphani, yense anthu ace adapatikanawo ndi Baala-Peori.

6. Ndipo, taonani, anadza wina wa ana a Israyeli, nabwera naye mkazi Mmidyani kudza naye kwa abale ace, pamaso pa Mose, ndi pamaso pa khamu lonse la ana a Israyeli, pakulira iwo pa khomo la cihema cokomanako.

7. Pamene Pinehasi mwana wa Eleazara, mwana wa Aroni wansembe, anaciona, anauka pakati pa khamu, natenga nthungo m'dzanja lace;

8. natsata munthu M-israyeli m'hema, nawamoza onse awiri, munthu M-israyeli ndi mkaziyo m'mimba mwace. Pamenepo mliri unaletseka kwa ana a Israyeli.

Werengani mutu wathunthu Numeri 25