Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 24:1-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Pamene Balamu anaona kuti kudakomera pamaso pa Yehova kudalitsa Israyeli, sanamuka, monga nthawi zija zina, ku nyanga zolodzera, koma anayang'ana nkhope yace kucipululu.

2. Ndipo Balamu anakweza maso ace, naona Israyeli alikukhala monga mwa mafuko ao; ndipo mzimu wa Mulungu unadza pa iye.

3. Pamenepo ananena fanizo lace, nati,Balamu mwana wa Beori anenetsa,Ndi munthuyo anatsinzina maso anenetsa;

4. Wakumva mau a Mulungu anenetsa,Wakuona masomphenya a Wamphamvuyonse,Wakugwa pansi maso ace openyuka:

5. Ha! mahema ako ngokoma, Yakobo;Zokhalamo zako, Israyeli!

6. Ziyalika monga zigwa,Monga minda m'mphepete mwanyanja,Monga khonje waoka Yehova,Monga mikungudza m'mphepete mwa madzi.

7. Madzi adzayenda naturuka m'zotungira zace,Ndi mbeu zace zidzakhala ku madzi ambiri,Ndi mfumu yace idzamveka koposa Agagi,Ndi ufumu wace udzamveketsa.

8. Mulungu amturutsa m'Aigupto;Ali nayo mphamvu yonga ya njati;Adzawadya amitundu, ndiwo adani ace.Nadzaphwanya mafupa ao, Ndi kuwapyoza ndi mibvi yace.

9. Anaunthama, nagona pansi ngati mkango,Ngati mkango waukazi; adzamuutsa ndani?Wodalitsika ali yense wakudalitsa iwe,Wotemberereka ali yense wakutemberera iwe.

Werengani mutu wathunthu Numeri 24