Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 24:1-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Pamene Balamu anaona kuti kudakomera pamaso pa Yehova kudalitsa Israyeli, sanamuka, monga nthawi zija zina, ku nyanga zolodzera, koma anayang'ana nkhope yace kucipululu.

2. Ndipo Balamu anakweza maso ace, naona Israyeli alikukhala monga mwa mafuko ao; ndipo mzimu wa Mulungu unadza pa iye.

3. Pamenepo ananena fanizo lace, nati,Balamu mwana wa Beori anenetsa,Ndi munthuyo anatsinzina maso anenetsa;

4. Wakumva mau a Mulungu anenetsa,Wakuona masomphenya a Wamphamvuyonse,Wakugwa pansi maso ace openyuka:

5. Ha! mahema ako ngokoma, Yakobo;Zokhalamo zako, Israyeli!

6. Ziyalika monga zigwa,Monga minda m'mphepete mwanyanja,Monga khonje waoka Yehova,Monga mikungudza m'mphepete mwa madzi.

7. Madzi adzayenda naturuka m'zotungira zace,Ndi mbeu zace zidzakhala ku madzi ambiri,Ndi mfumu yace idzamveka koposa Agagi,Ndi ufumu wace udzamveketsa.

8. Mulungu amturutsa m'Aigupto;Ali nayo mphamvu yonga ya njati;Adzawadya amitundu, ndiwo adani ace.Nadzaphwanya mafupa ao, Ndi kuwapyoza ndi mibvi yace.

9. Anaunthama, nagona pansi ngati mkango,Ngati mkango waukazi; adzamuutsa ndani?Wodalitsika ali yense wakudalitsa iwe,Wotemberereka ali yense wakutemberera iwe.

10. Pamenepo Balaki anapsa mtima pa Balamu, naomba m'manja; ndipo Balaki anati kwa Balamu, Ndinakuitana kutemberera adani ansa, ndipo unawadalitsa ndithu katatu tsopano.

11. Cifukwa cace thawira ku malo ako tsopano; ndikadakucitira ulemu waukuru; koma, taona, Yehova wakuletsera ulemu.

12. Ndipo Balamu anati kwa Balaki, Kodi sindinauzanso amithenga anu amene munawatumiza kwa ine, ndi kuti,

13. Cinkana Balaki akandipatsa nyumba yace yodzala ndi siliva ndi golidi, sindikhoza kutumpha mau a Yehova, kucita cokoma kapena coipa ine mwini wace; conena Yehova ndico ndidzanena ine?

Werengani mutu wathunthu Numeri 24