Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 23:13-27 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. Ndipo Balaki anati naye, Tiyetu, upite nane kumalo kwina, kumene ukawaona; udzaona malekezero ao okha, osawaona onse; ndipo pokhala pamenepo ukanditembererere iwo.

14. Ndipo anamuka naye ku thengo la Zofimu, pamwamba pa Pisiga, namangako maguwa a nsembe asanu ndi awiri, napereka ng'ombe ndi nkhosa pa guwa la nsembe liri lonse.

15. Ndipo anati kwa Balaki, Imani pano pa nsembe yopsereza yanu, ndipite ine ndikakomane ndi iye uko.

16. Ndipo Yehova anakomana naye Balamu, naika mau m'kamwa mwace, nati, Bwerera kwa Balaki, nukanene cakuti cakuti.

17. Ndipo anadza kuli iye, ndipo taona, analikuima pa nsembe yace yopsereza, ndi akalonga a Moabu pamodzi naye. Ndipo Balaki anati kwa iye, Wanenanji Yehova?

18. Ndipo ananena fanizo lace, nati,Ukani, Balaki, imvani;Ndimvereni, mwana wa Zipori;

19. Mulungu sindiye munthu, kuti aname;Kapena mwana wa munthu, kuti aleke;Kodi anena, osacita?

20. Kapena kulankhula, osacitsimikiza?Taonani, ndalandira mau akudalitsa,Popeza iye wadalitsa, sinditha kusintha.

21. Sayang'anira mphulupulu iri m'Yakobo,Kapena sapenya kupulukira kuli m'lsrayeli.Yehova Mulungu wace ali ndi iye,Ndi mpfuu wa mfumu uli pakati pao,

22. Mulungu awaturutsa m'Aigupto;Mphamvu yace ikunga ya njati.

23. Pakuti palibe nyanga pakati pa Yakobo,Kapena ula mwa Israyeli;Pa nyengo yace adzanena kwa Yakobo ndi Israyeli,Cimene Mulungu acita.

24. Taonani, anthuwo auka ngati mkango waukazi,Nadzitukumula ngati mkango waumuna:Sugonansokufikira utadya nyama yogwira,Utamwa mwazi wa zophedwa.

25. Ndipo Balaki anati kwa Balamu, Usawatemberera konse, kapena kuwadalitsa konse.

26. Koma Balamu anayankha nati kwa Balaki, Sindinakuuzani ndi kuti, Ciri conse acinena Yehova, comweco ndizicita?

27. Ndipo Balaki anati kwa Balamu, Tiyetu, ndimuke nawe kumalo kwina; kapena kudzakomera pamaso pa Mulungu kuti unditembererere iwo pokhala kumeneko.

Werengani mutu wathunthu Numeri 23