Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 23:1-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Balamu anati kwa Balaki, Ndimangireni kuno maguwa a nsembe asanu ndi awiri, nimundikonzere kuno ng'ombe zisanu ndi ziwiri, ndi nkhosa zamphongo zisanu ndi ziwiri.

2. Ndipo Balaki anacita monga Balamu ananena; ndipo Balaki ndi Balamu anapereka pa guwa la nsembe liri lonse ng'ombe ndi nkhosa yamphongo.

3. Ndipo Balamu anati kwa Balaki, Imani pa nsembe yopsereza yanu, ndipite ine, kapena Yehova akadza kukomana ndi ine; ndipo cimene akandionetsa ine ndidzakufotokozerani. Ndipo anapita pamsanje poyera,

4. Pamenepo Mulungu anakomana ndi Balamu; ndipo ananena ndi iye, Ndakonza maguwa a nsembe asanu ndi awiri, ndipo ndapereka ng'ombe ndi nkhosa yamphongo pa guwa la nsembe liri lonse.

5. Ndipo Yehova anaika mau m'kamwa mwa Balamu, nati, Bwerera kwa Balaki, nukanene cakuti cakuti.

6. Ndipo anabwerera kwa iye, ndipo, taonani, analikuima pa nsembe yopsereza yace, iye ndi akalonga onse a Moabu.

7. Ndipo ananena fanizo lace, nati,Ku Aramu ananditenga Balaki,Mfumu ya Moabu ananditenga ku mapiri a kum'mawa;Idza, udzanditembererere Yakobo.Idza, nudzanyoze Israyeli.

8. Ndidzatemberera bwanji amene Mulungu sanamtemberera?Ndidzanyoza bwanji, amene Yehova sanamnyoza?

Werengani mutu wathunthu Numeri 23