Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 22:17-28 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

17. popeza ndidzakucitira ulemu waukuru, ndipo zonse unena ndi ine ndidzacita; cifukwa cace idzatu, unditembererere anthu awa.

18. Ndipo Balamu, anayankha nati kwa anyamata a Balaki, Cinkana Balaki andipatsa nyumba yace yodzala ndi siliva ndi golidi, sindikhoza kutumpha mau a Yehova Mulungu wanga, kucepsako kapena kuonjezako.

19. Ndikupemphani, tsono, khalani pano inu usiku uno womwe; kuti ndidziwe comwe Yehova adzanenanso nane.

20. Ndipo Mulungu anadza kwa Balamu usiku, nanena naye, Akadza kukuitana anthuwa, nyamuka, kumka nao, koma mau okha okha ndinena ndi iwe, ndiwo ukacite.

21. Pamenepo Balamu anauka m'mawa namanga buru wace, namuka nao akalonga a ku Moabu.

22. Koma anapsa mtima Mulungu cifukwa ca kupita iye, ndipo mthenga wa Yehova anadziika m'njira wotsutsana naye, Ndipo anali wokwera pa buru wace, ndi anyamata ace awiri anali naye,

23. Ndipo buruyo anaona mthenga wa Yehova alikuima m'njira, ndi lupanga lace ku dzanja lace; ndi buru anapatuka m'njira, nalowa kuthengo; ndipo Balamu anampanda buru kumbwezera kunjira.

24. Pamenepo mthenga wa Yehova anaima m'njira yopapatiza ya minda yampesa; mbali yina kuli linga, mbali yina linga.

25. Ndipo buru anaona mthenga wa Yehova, nadzikankhira kulinga, nakanikiza phazi la Balamu kulinga; ndipo anampandanso.

26. Pamenepo mthenga wa Yehova anapitiriranso, naima popapatiza, popanda popatukira kulamanja kapena kulamanzere.

27. Ndipo buru wace anaona mthenga wa Yehova, nagona pansi, Balamu ali pamsana pace; ndipo Balamu adapsa mtima, nampanda buru ndi ndodo.

28. Ndipo Yehova anatsegula pakamwa pace pa buru, nati uyu kwa Balamu, Ndakucitanji, kuti wandipanda katatu tsopano?

Werengani mutu wathunthu Numeri 22