Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 2:7-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. Ndi pfuko la Zebuloni: kalonga wa ana a Zebuloni ndiye Eliyabu mwana wa Heloni.

8. Ndi khamu lace, ndi owerengedwa ace, ndiwo zikwi makumi asanu mphambu zisanu ndi ziwiri kudza mazana anai.

9. Owerengedwa onse a cigono ca Yuda ndiwo zikwi makumi khumi mphambu makumi asanu ndi atatu kudza zisanu ndi cimodzi mphambu mazana anai, monga mwa makamu ao, Ndiwo azitsogolera ulendo.

10. Mbendera ya cigono ca Rubeni ikhale kumwera monga mwa makamu ao; ndipo kalonga wa ana a Rubeni ndiye Elizuri mwana wa Sedeuri.

11. Ndi khamu lace, ndi olembedwa ace, ndiwo zikwi makumi anai mphambu zisanu ndi cimodzi kudza mazana asanu.

12. Ndipo iwo akumanga mahema ao poyandikizana naye ndiwo a pfuko la Simeoni; ndi kalonga wa ana a Simeoni ndiye Selumiyeli mwana wa Surisadai.

13. Ndi khamu lace ndi owerengedwa ace, ndiwo zikwi makumi asanu mphambu zisanu ndi zinai kudza mazana atatu.

14. Ndi pfuko la Gadi; kalonga wa ana a Gadi ndiye Eliyasafe mwana wa Reueli.

15. Ndi khamu lace, ndi owerengedwa ace, ndiwo zikwi makumi anai mphambu zisanu kudza mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi asanu.

16. Owerengedwa onse a cigono ca Rubeni ndiwo zikwi makumi khumi mphambu makumi asanu ndi cimodzi kudza mazana anai mphambu makumi asanu, monga mwa makamu ao. Ndiwo azitsatana nao otsogolerawo.

17. Pamenepo khamu la Alevi azimuka naco cihema cokomanako, pakati pa makamu; monga amamanga mahema ao, momwemo azimuka ulendo wao, munthu yense pamalo pace, monga mwa mbendera zao.

18. Mbendera ya cigono ca Efraimu izikhala kumadzulo monga mwa makamu ao; ndipo kalonga wa ana a Efraimu ndiye Elisama mwana wa Amihudi.

19. Ndi khamu lace, ndi owerengedwa ace, ndiwo zikwi makumi anai kudza mazana asanu.

20. Ndipo oyandikizana naye ndiwo a pfuko la Manase; ndi kalonga wa ana a Manase ndiye Gamaliyeli mwana wa Pedazuri.

Werengani mutu wathunthu Numeri 2