Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 2:16-27 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

16. Owerengedwa onse a cigono ca Rubeni ndiwo zikwi makumi khumi mphambu makumi asanu ndi cimodzi kudza mazana anai mphambu makumi asanu, monga mwa makamu ao. Ndiwo azitsatana nao otsogolerawo.

17. Pamenepo khamu la Alevi azimuka naco cihema cokomanako, pakati pa makamu; monga amamanga mahema ao, momwemo azimuka ulendo wao, munthu yense pamalo pace, monga mwa mbendera zao.

18. Mbendera ya cigono ca Efraimu izikhala kumadzulo monga mwa makamu ao; ndipo kalonga wa ana a Efraimu ndiye Elisama mwana wa Amihudi.

19. Ndi khamu lace, ndi owerengedwa ace, ndiwo zikwi makumi anai kudza mazana asanu.

20. Ndipo oyandikizana naye ndiwo a pfuko la Manase; ndi kalonga wa ana a Manase ndiye Gamaliyeli mwana wa Pedazuri.

21. Ndi khamu lace, ndi owerengedwa ace, ndiwo zikwi makumi atatu mphambu ziwiri kudza mazana awiri.

22. Ndi pfuko la Benjamini: kalonga wa ana a Benjamini ndiye Abidana mwana wa Gideoni.

23. Ndi khamu lace, ndi owerengedwa ace, ndiwo zikwi makumi atatu mphambu zisanu kudza mazana anai.

24. Owerengedwa onse a cigono ca Efraimu ndiwo zikwi makumi khumi mphambu zisanu ndi zitatu kudza zana limodzi, monga mwa makamu ao. Iwo ndiwo aziyenda gulu lacitatu paulendo.

25. Mbendera ya cigono ca Dani izikhala kumpoto monga mwa makamu ao; ndi kalonga wa ana a Dani ndiye Ahiyezeri mwana wa Amisadai.

26. Ndi khamu lace, ndi owerengedwa ace, ndiwo zikwi makumi asanu ndi limodzi mphambu ziwiri kudza mazana asanu ndi awiri.

27. Ndipo iwo akumanga mahema ao poyandikizana naye ndiwo a pfuko la Aseri; ndi kalonga wa ana a Aseri ndiye Pagiyeli mwana wa Okirani.

Werengani mutu wathunthu Numeri 2