19. Ndipo woyerayo awaze pa wodetsedwayo tsiku lacitatu, ndi tsiku lacisanu ndi ciwiri; ndipo tsiku lacisanu ndi ciwiri amyeretse; ndipo atsuke zobvala zace, nasambe m'madzi, nadzakhala woyera madzulo.
20. Koma munthu wakukhala wodetsedwa, koma wosadziyeretsa, azimsadza munthuyo pakati pa msonkhano, popeza waipsa malo opatulika a Yehova; sanamwaza madzi akusiyanitsa; ndiye wodetsedwa.
21. Ndipo likhale kwa iwo lemba losatha; kuti iye wakuwaza madzi akusiyanitsa azitsuka zobvala zace; ndi iye wakukhudza madzi akusiyanitsa adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.
22. Ndipo ciri conse munthu wodetsedwa acikhudza cidzakhala codetsedwa; ndi munthu wakucikhudza adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.