Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 19:1-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, nati,

2. Ili ndi lemba la cilamulo Yehova adalamuliraci, ndi kuti, Nena ndi ana a Israyeli kuti azikutengera ng'ombe ramsoti yofiira, yangwiro yopanda enema, yosamanga m'goli;

3. ndipo muipereke kwa Eleazara wansembe, naiturutse iye kunja kwa cigono, ndipo wina aiphe pamaso pace.

4. Ndipo Eleazara wansembe atengeko mwazi wace ndi cala cace, nawazeko mwazi wace kasanu ndi kawiri pakhomo pa cihema cokomanako.

5. Pamenepo atenthe ng'ombe yamsotiyo pamaso pace; atenthe cikopa cace ndi nyama yace, ndi mwazi wace, pamodzi ndi cipwidza cace.

6. Ndipo wansembe atenge mtengo wamkungudza, ndi hisope, ndi ubweya wofiira, naziponye pakati pa mota irikupsererapo ng'ombe yamsoti.

7. Pamenepo wansembe atsuke zobvala zace, nasambe thupi lace ndi madzi; ndipo atatero alowenso kucigono; koma wansembeyo adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.

8. Ndipo iye wakutentha ng'ombeyo atsuke zobvala zace, nasambe thupi lace ndi madzi, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.

9. Ndipo munthu woyera aole mapulusa a ng'ombe ya msotiyo, nawaike kunja kwa cigono, m'malo moyera: ndipo awasungire khamu la ana a lsrayeli akhale a madzi akusiyanitsa; ndiwo nsembe yaucimo.

10. Ndipo wakuola mapulusayo a ng'ombe ya msoti atsuke zobvala zace, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo; ndipo likhale lemba losatha kwa ana a Israyeli, ndi kwa mlendo wakukhala pakati pao.

11. Iye wakukhudza mtembo wa munthu ali yense adzakhala wodetsedwa masiku asanu ndi awiri;

Werengani mutu wathunthu Numeri 19