Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 16:42-50 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

42. Ndipo kunali, posonkhanidwa khamulo kutsutsana nao Mose ndi Aroni, kuti anaceukira cihema cokomanako; taonani, mtambo unaciphimba, ndi ulemerero wa Yehova unaoneka.

43. Ndipo Mose ndi Aroni anadza kukhomo kwa cihema cokomanako.

44. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,

45. Kwerani kucoka pakati pa khamu lino, kuti ndiwathe m'kamphindi. Pamenepo adagwa nkhope zao pansi.

46. Ndipo Mose anati kwa Aroni, Tenga mbale yako yofukiza, nuikemo mota wa ku guwa la nsembe, nuikepo cofukiza, nufulumire kumuka ku khamulo, nuwacitire cowatetezera; pakuti waturuka mkwiyo pamaso pa Yehova; wayamba mliri.

47. Ndipo Aroni anatenga monga Mose adanena, nathamanga kulowa pakati pa msonkhano; ndipo taonani, udayamba mliri pakati pa anthu; ndipo anaikapo cofukiza nawacitira anthu cowatetezera.

48. Ndipo anaima pakati pa akufa ndi amoyo; ndi mliri unaleka.

49. Koma akufa nao mliri ndiwo zikwi khumi ndi zinai mphambu mazana asanu ndi awiri, osawerenga aja adafera cija ca Kora.

50. Ndipo Aroni anabwera kwa Mose ku khomo la cihema cokomanako; ndi mliri unaleka.

Werengani mutu wathunthu Numeri 16