Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 16:26-37 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

26. Ndipo ananena ndi khamulo, nati, Cokanitu ku mahema a anthu awa oipa, musamakhudza kanthu kao kali konse, mungaonongeke m'zocimwa zao zonse.

27. Potero anakwera kucokera pozungulira mahema a Kora, Datani, ndi Abiramu, ndipo Datani ndi Abiramu anaturuka, naima pakhomo pa mahema ao, ndi akazi ao, ndi ana ao amuna, ndi makanda ao.

28. Ndipo Mose anati, Ndi ici mudzadziwa kuti Yehova wanditumiza ine kucita nchito izi zonse, ndi kuti sizifuma m'mtima mwanga mwanga.

29. Akafa anthu awa monga amafa anthu onse, kapena akasungika monga amasungika anthu onse, Yehova sananditumiza ine.

30. Koma Yehova akalenga cinthu catsopano, ndi nthaka ikayasama pakamwa pace, nikawameza ndi zonse ali nazo, nakatsikira iwo kumanda ali ndi moyo; pamenepo mudzadziwa kuti anthu awa anyoza Mulungu.

31. Ndipo kunali, pakutha iye kunena mau awa onse, nthaka inang'ambika pansi pao;

32. ndi dziko linayasama pakamwa pace ndi kuwameza, iwo ndi mabanja ao, ndi amuna ao onse akutsata Kora, ndi akatundu ao onse.

33. Comweco iwowa, ndi onse anali nao, anatsikira kumanda ali ndi moyo, ndi dziko linasunama pa iwo, ndipo anaonongeka pakati pa msonkhano.

34. Ndipo Aisrayeli onse akukhala pozinga pao anathawa pakumva kupfuula kwao; pakuti anati, Lingatimeze dziko ifenso.

35. Ndipo mota unaturuka kwa Yehova, ndi kunyeketsa amuna mazana awiri ndi makumi asanu aja akubwera naco cofukiza.

36. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,

37. Nena ndi Eleazara mwana wa Aroni wansembe, kuti aphule mbale zofukiza pakati pa moto, nutaye makalawo uko kutali; pakuti ziri zopatulika;

Werengani mutu wathunthu Numeri 16