Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 15:9-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. abwere nayo, pamodzi ndi ng'ombeyo, nsembe ya ufa wosalala, atatu mwa magawo khumi wosanganiza ndi mafuta, limodzi la magawo awiri la bini.

10. Ndipo ubwere naye vinyo wa nsembe yothira limodzi la magawo awiri la hini, ndiye nsembe yamoto ya pfungo: lokoma, ya Yehova.

11. Kudzatero ndi ng'ombe iri yonse, kapena nkhosa yamphongo iri yonse, kapena mwana wa nkhosa ali yense, kapena mwana wa mbuzi ali yense.

12. Monga mwa kuwerenga kwace kwa izi muzikonza, muzitero ndi yonse monga mwa kuwerenga kwace.

13. Onse akubadwa m'dzikomo acite izi momwemo, pobwera nayo kwa Yehova nsembe yamoto ya pfungo lokoma.

14. Ndipo akakhala nanu mlendo, kapena ali yense wakukhala pakati pa inu mwa mibadwo yanu, nakacitira Yehova nsembe yamoto ya pfungo lokoma; monga mucita inu, momwemo iyenso,

15. Kunena za khamu, pakhale lemba limodzi kwa inu, ndi kwa mlendo wakukhala kwanu, ndilo lemba losatha mwa mibadwo yanu; monga mukhala inu, momwemo mlendo pamaso pa Yehova.

16. Pakhale cilamulo cimodzi ndi ciweruzo cimodzi kwa inu ndi kwa mlendo wakukhala kwanu.

17. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,

18. Nena ndi ana a Israyeli, nuti nao, Pamene mulowa m'dziko limene ndirikukulowetsani,

19. kudzali, pakudya inu mkate wa m'dzikolo, muzikwezera Yehova nsembe yokweza.

20. Pa mtanda wanu woyamba muperekeko kamtanda, kakhale nsembe yokweza; monga mumacitira nsembe yokweza ya popuntha tirigu, momwemo muzikakweza.

21. Muzipatsa Yehova nsembe yokweza yoitenga ku mtanda wanu woyamba, mwa mibadwo yanu.

Werengani mutu wathunthu Numeri 15