Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 15:34-41 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

34. Ndipo anathanga wamsunga, popeza sicinanenedwa coyenera kumcitira iye.

35. Ndipo Yehova anati kwa Mose, Amuphe munthuyu ndithu; khamu lonse limponye miyala kunja kwa cigono.

36. Pamenepo khamu lonse linamturutsa kunja kwa cigono, ndi kumponya miyala, ndipo anafa; monga Yehova adauza Mose.

37. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,

38. Nena ndi ana a Israyeli, nuwauze kuti adziombere mphonje m'mphepete mwa zobvala zao, mwa mibadwo yao, naike pamphonje m'mphepetemo thonje lamadzi.

39. Ndipo cikhale kwa inu mphonje, yakuti muziyang'anirako, ndi kukumbukila malamulo onse a Yehova, ndi kuwacita, ndi kuti musamazondazonda kutsata za m'mtima mwanu, ndi za m'maso mwanu zimene mumatsata ndi cigololo;

40. kuti mukumbukile ndi kucita malamulo anga onse, ndi kukhala wopatulikira Mulungu wanu.

41. Ine ndine Yehova Mulungu wanu, wakukuturutsani m'dziko la Aigupto, kuti ndikhale Mulungu wanu; Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

Werengani mutu wathunthu Numeri 15