Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 15:16-24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

16. Pakhale cilamulo cimodzi ndi ciweruzo cimodzi kwa inu ndi kwa mlendo wakukhala kwanu.

17. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,

18. Nena ndi ana a Israyeli, nuti nao, Pamene mulowa m'dziko limene ndirikukulowetsani,

19. kudzali, pakudya inu mkate wa m'dzikolo, muzikwezera Yehova nsembe yokweza.

20. Pa mtanda wanu woyamba muperekeko kamtanda, kakhale nsembe yokweza; monga mumacitira nsembe yokweza ya popuntha tirigu, momwemo muzikakweza.

21. Muzipatsa Yehova nsembe yokweza yoitenga ku mtanda wanu woyamba, mwa mibadwo yanu.

22. Ndipo pamene mulakwa, osacita mau awa onse amene Yehova ananena ndi Mose;

23. ndizo zonse Yehova anakuuzani ndi dzanja la Mose, kuyambira tsikulo Yehova anauza, ndi kunkabe m'mibadwo yanu;

24. pamenepo kudzali, ngati anacicita osati dala, osacidziwa khamulo, khamu lonse lipereke ng'ombe yamphongo ikhale nsembe yopsereza, ya pfungo lokoma ya Yehova, pamodzi ndi nsembe yace yaufa, ndi nsembe yace yothira, monga mwa ciweruzo cace; ndi tonde mmodzi akhale nsembe yaucimo.

Werengani mutu wathunthu Numeri 15