Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 15:1-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Yehova ananena ndi Mose nati,

2. Nena ndi ana a Israyeli, nuti nao, Mukakalowa m'dziko lokakhalamo inu, limene ndirikupatsa inu,

3. ndipo mukakonzera Yehova nsembe yamoto, nsembe yopsereza, kapena yophera, pocita cowinda ca padera, kapena nsembe yaufulu, kapena nsembe ya pa nyengo zanu zoikika, kumcitira Yehova pfungo lokoma, la ng'ombe kapena nkhosa;

4. pamenepo iye wobwera naco copereka cace kwa Yehova, azibwera nayo nsembe yaufa, limodzi la magawo khumi la ufa wosalala, wosanganiza ndi limodzi la magawo anai la bini la mafuta;

5. ndipo uzikonzera nsembe yopsereza kapena yophera, vinyo wa nsembe yothira, limodzi la magawo anai la bini, ukhale wa mwana wa nkhosa mmodzi.

6. Kapena ukonzere nkhosa yamphongo nsembe yaufa, awiri mwa magawo khumi a ufa wosalala, wosanganiza ndi mafuta, limodzi la magawo atatu la bini.

7. Ndipo ubwere naye vinyo wa nsembe yothira, limodzi la magawo atatu la bini, acitire Yehova pfungo lokoma.

8. Ndipo pamene mukonza ng'ombe ikhale nsembe yopsereza, kapena yophera, kucita cowinda ca padera, kapena ikhale nsembe yoyamika ya Yehova;

9. abwere nayo, pamodzi ndi ng'ombeyo, nsembe ya ufa wosalala, atatu mwa magawo khumi wosanganiza ndi mafuta, limodzi la magawo awiri la bini.

10. Ndipo ubwere naye vinyo wa nsembe yothira limodzi la magawo awiri la hini, ndiye nsembe yamoto ya pfungo: lokoma, ya Yehova.

Werengani mutu wathunthu Numeri 15