Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 14:1-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Pamenepo khamu lonse linakweza mau ao, napfuula; ndipo anthuwo analira usikuwo.

2. Ndipo ana onse a Israyeli anadandaulira Mose ndi Aroni; ndi khamu lonse linanena nao, Mwenzi tikadafa m'dziko la Aigupto; kapena mwenzi tikadafa m'cipululu muno!

3. Ndipo Yehova atitengeranii kudza nafe kudziko kuno, kuti tigwe nalo lupanga? Akazi athu ndi makanda athu adzakhala cakudya cao; kodi sikuli bwino tibwerere ku Aigupto?

4. Ndipo anati wina ndi mnzace, Tiike mtsogoleri, tibwerere ku Aigupto.

5. Pamenepo Mose ndi Aroni anagwa nkhope pansi pamaso pa msonkhano wonse wa khamu la ana a Israyeli.

6. Ndipo Yoswa mwana wa Nuni, ndi Kalebi mwana wa Yefune, ndiwo a iwo aja adazonda dzikolo, anang'amba zobvala zao;

7. nanena ndi khamu lonse la ana a Israyeli, nati, Dziko tapitamo kulizonda, ndilo dziko lokometsetsa ndithu.

8. Yehova akakondwera nafe, adzatilowetsa m'dzikomo, ndi kutipatsa ilo; ndilo dziko moyenda mkaka ndi uci ngati madzi.

9. Cokhaci musamapikisana naye Yehova, musamaopa anthu a m'dzikomo; pakuti ndiwo mkate wathu; mthunzi wao wawacokera, ndipo Yehova ali nafe; musamawaopa.

Werengani mutu wathunthu Numeri 14