Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 14:29-41 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

29. mitembo yanu idzagwa m'cipululu muno; ndi owerengedwa anu onse, monga mwa kuwerenga kwanu konse, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, akudandaula pa Ine;

30. simudzalowa inu m'dzikolo, ndinakwezapo dzanja langa kukukhalitsani m'mwemo, koma Kalebi mwana wa Yefune, ndi Yoswa mwana wa Nuni ndiwo.

31. Koma makanda anu, amene munanena za iwowa kuti adzakhala cakudya, amenewo ndidzavalowetsa, ndipo adzadziwa dzikolo mudalikana.

32. Koma inu, mitembo yanu idzagwa m'cipululu muno.

33. Ndipo ana anu adzakhala oyendayenda m'cipululu zaka makumi anai, nadzasenza kupulukira kwanu, kufikira mitembo yanu yatha m'cipululu.

34. Monga mwa kuwerenga kwa masiku amene munazonda dziko, masiku makumi anai, tsiku limodzi kuwerenga caka cimodzi, mudzasenza mphulupulu zanu, zaka makumi anai, ndipo mudzadziwa kuti ndaleka lonjezano langa.

35. Ine Yehova ndanena, ndidzacitira ndithu ici khamu ili lonse loipa lakusonkhana kutsutsana nane; adzatha m'cipululu muno, nadzafamo.

36. Ndipo amunawo, amene Mose anawatumiza kukazonda dziko, amene anabwera nadandaulitsa khamu lonse pa iye, poipsa mbiri ya dziko,

37. amuna amene anaipsa mbiri ya dziko, anafa ndi mliri pamaso pa Yehova.

38. Koma Yoswa mwana wa Nuni, ndi Kalebi mwana wa Yefune, anakhala ndi moyo mwa amuna aja adamukawo kukazonda dziko.

39. Ndipo Mose anauza ana a Israyeli mao onse awa; ndipo anthu anamva cisoni cambiri.

40. Ndipo anauka mamawa, nakwera pamwamba pa, phiri, nati, Tiri pano, tidzakwera kumka ku malo amene Yehova ananena; popeza tacimwa.

41. Ndipo Mose anati, Mutero cifukwa ninji kulakwira mau a Yehova, popeza simudzapindula nako?

Werengani mutu wathunthu Numeri 14