Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 14:24-38 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

24. koma mtumiki wanga Kalebi, popeza anali nao mzimu wina, nanditsata monsemo, ndidzamlowetsa iyeyu m'dziko muja analowamo; ndi mbeu zace zidzakhala nalo.

25. Koma Aamaleki ndi Akanani akhala m'cigwamo; tembenukani mawa, nimumke ulendo wanu kucipululu, njira ya ku Nyanja Yofiira.

26. Ndipo Yehova ananena kwa Mose ndi Aroni, nati,

27. Ndileke khamu loipa ili lakudandaula pa Ine kufikira liti? Ndidamva madandaulo a ana a Israyeli, amene amandidandaulira.

28. Nunene nao, Pali Ine, ati Yehova, ndidzacitira inu ndithu monga mwanena m'makutu mwanga;

29. mitembo yanu idzagwa m'cipululu muno; ndi owerengedwa anu onse, monga mwa kuwerenga kwanu konse, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, akudandaula pa Ine;

30. simudzalowa inu m'dzikolo, ndinakwezapo dzanja langa kukukhalitsani m'mwemo, koma Kalebi mwana wa Yefune, ndi Yoswa mwana wa Nuni ndiwo.

31. Koma makanda anu, amene munanena za iwowa kuti adzakhala cakudya, amenewo ndidzavalowetsa, ndipo adzadziwa dzikolo mudalikana.

32. Koma inu, mitembo yanu idzagwa m'cipululu muno.

33. Ndipo ana anu adzakhala oyendayenda m'cipululu zaka makumi anai, nadzasenza kupulukira kwanu, kufikira mitembo yanu yatha m'cipululu.

34. Monga mwa kuwerenga kwa masiku amene munazonda dziko, masiku makumi anai, tsiku limodzi kuwerenga caka cimodzi, mudzasenza mphulupulu zanu, zaka makumi anai, ndipo mudzadziwa kuti ndaleka lonjezano langa.

35. Ine Yehova ndanena, ndidzacitira ndithu ici khamu ili lonse loipa lakusonkhana kutsutsana nane; adzatha m'cipululu muno, nadzafamo.

36. Ndipo amunawo, amene Mose anawatumiza kukazonda dziko, amene anabwera nadandaulitsa khamu lonse pa iye, poipsa mbiri ya dziko,

37. amuna amene anaipsa mbiri ya dziko, anafa ndi mliri pamaso pa Yehova.

38. Koma Yoswa mwana wa Nuni, ndi Kalebi mwana wa Yefune, anakhala ndi moyo mwa amuna aja adamukawo kukazonda dziko.

Werengani mutu wathunthu Numeri 14