Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 14:22-29 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

22. popeza anthu onse awa amene adaona ulemerero wanga, ndi zizindikilo zanga, ndidazicita m'Aigupto ndi m'cipululu, koma anandiyesa Ine kakhumi aka, osamvera mau anga;

23. sadzaona dzikoli ndidalumbirira makolo ao, ngakhale mmodzi wa iwo akundinyoza Ine, sadzaliona;

24. koma mtumiki wanga Kalebi, popeza anali nao mzimu wina, nanditsata monsemo, ndidzamlowetsa iyeyu m'dziko muja analowamo; ndi mbeu zace zidzakhala nalo.

25. Koma Aamaleki ndi Akanani akhala m'cigwamo; tembenukani mawa, nimumke ulendo wanu kucipululu, njira ya ku Nyanja Yofiira.

26. Ndipo Yehova ananena kwa Mose ndi Aroni, nati,

27. Ndileke khamu loipa ili lakudandaula pa Ine kufikira liti? Ndidamva madandaulo a ana a Israyeli, amene amandidandaulira.

28. Nunene nao, Pali Ine, ati Yehova, ndidzacitira inu ndithu monga mwanena m'makutu mwanga;

29. mitembo yanu idzagwa m'cipululu muno; ndi owerengedwa anu onse, monga mwa kuwerenga kwanu konse, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, akudandaula pa Ine;

Werengani mutu wathunthu Numeri 14