Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 13:28-33 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

28. Komatu anthu okhala m'dzikomo ngamphamvu; ndi midziyo nja malinga, yaikuru ndithu: ndipo tinaonakonso ana a Anaki.

29. Aamaleke akhala m'dziko la kumwera; ndi Ahiti, ndi Ayebusi, ndi Aamori, akhala ku mapiri, ndi Akanani akhala kunyanja, ndi m'mphepete mwa Yordano.

30. Koma Kalebi anatontholetsa anthu pamaso pa Mose, nati, Tikwere ndithu ndi kulilandira lathu lathu; popeza tikhozadi kucita kumene.

31. Koma anthu adakwera nayewo anati, Sitikhoza kuwakwerera anthuwo; popeza atiposa mphamvu,

32. Ndipo anaipsira ana a Israyeli mbiri ya dziko adalizonda, nati, Dzikoli tapitamo kulizonda, ndilo dziko lakutheramo anthu okhalamo; ndi anthu onse tidaona pakati pace ndiwo anthu atali misinkhu.

33. Tinaonakonso Anefili, ana a Anaki, obadwa ndi Anefili; ndipo tinaoneka m'maso mwathu ngati zinsidzi; momwemonso tinaoneka m'maso mwao.

Werengani mutu wathunthu Numeri 13