Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 12:13-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. Ndipo Mose anapfuulira kwa Yehova, ndi kuti, Mciritsenitu, Mulungu,

14. Ndipo Yehova anati kwa Mose, Atate wace akadamlabvulira malobvu pankhope pace sakadacita manyazi masiku asanu ndi awiri? ambindikiritse kunja kwa cigono masiku asanu ndi awiri; ndipo atatero amlandirenso.

15. Pamenepo anambindikiritsa Miriamu kunja kwa cigono masiku asanu ndi awiri; ndipo anthu sanayenda ulendo kufikira atamlandiranso Miriamu.

16. Ndipo atatero anthuwo anamka ulendo wao kucokera ku Hazeroti, namanga mahema ao m'cipululu ca Parana.

Werengani mutu wathunthu Numeri 12