Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 11:31-35 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

31. Ndipo kudacokera mphepo kwa Yehova, nidza nazo zinziri zocokera kunyanja, nizitula kucigono, ulendo wa tsiku limodzi dera lino, ndi ulendo wa tsiku limodzi dera lina, pozungulira pa cigono, ndipo zinabisa nthaka ngati muyeso wa mikono iwiri.

32. Ndipo anthu anauka tsiku lonselo, ndi usiku wace wonse, ndi mawa lace lonse, nakusa zinzirizo; wokusa pang'ono anakusa zodzaza mahomeri khumi; ndipo anadziyanikira izi pozungulira pa cigono.

33. Nyamayi ikali pakati pa mano, asanaitafune, Mulungu anapsa mtima pa anthuwa, ndipo Yehova anawakantha anthu ndi kukantha kwakukuru ndithu.

34. Ndipo anacha malowo dzina lace Kibiroti Hatava; popeza pamenepo anaika anthu osusuka.

35. Kucokera ku Kibiroti Hatava anthuwo anayenda kumka ku Hazeroti; nakhala ku Hazeroti.

Werengani mutu wathunthu Numeri 11