20. Ndi pa gulu la pfuko la ana a Gadi anayang'anira Eliyasafe mwana wa Deyueli.
21. Pamenepo Akohati anayenda, ndi kunyamula zopatulika, ndi enawo anautsiratu kacisi asanafike iwowa.
22. Ndipo anayenda a mbendera ya cigono ca ana a Efraimu, monga mwa magulu ao; ndi pa gulu lace anayang'anira Elizama mwana wa Amihudi.
23. Ndi pa gulu la pfuko la ana a Manase anayang'anira Gamaliyeli mwana wa Pedazuri.
24. Ndi pa gulu la pfuko la ana a Benjamini anayang'anira Abidana mwana wa Gideoni.
25. Pamenepo anayenda a mbendera ya cigono ca ana a Dani, ndiwo a m'mbuyombuyo a zigono zonse, monga mwa magulu ao; ndi pa gulu lace anayang'anira Ahiyezeri mwana wa Amisadai.
26. Ndi pa gulu la pfuko la ana a Aseri anayang'anira Pagiyeli mwana wa Okirani.
27. Ndi pa gulu la pfuko la ana a Nafitali anayang'anira Ahira mwana wa Enani.
28. Potero maulendo a ana a Israyeli anakhala monga mwa magulu ao; nayenda ulendowao.
29. Ndipo Mose anati kwa Hobabu mwana wa Reueli Mmidyani mpongozi wa Mose, Ife tirikuyenda kumka ku malo amene Yehova anati, Ndidzakupatsani awa; umuke nafe, tidzakucitira zokoma; popeza Yehova wanenera Israyeli zokoma.
30. Koma anati kwa iye, Sindidzamuka nanu; koma ndipita ku dziko langa, ndi kwa abale anga.