Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Nehemiya 9:34-38 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

34. ndi mafumu athu, akuru athu, ansembe athu, ndi makolo athu, sanasunga cilamulo canu, kapena kumvera malamulo anu, ndi mboni zanu, zimene munawacitira umboni nazo.

35. Popeza sanatumikira Inu m'ufumu wao, ndi m'ubwino wanu wocuruka umene mudawapatsa, ndi m'dziko lalikuru ndi la zonona mudalipereka pamaso pao, ndipo sanabwerera kuleka nchito zao zoipa.

36. Tapenyani, ife lero ndife akapolo, ndi dzikoli mudalipereka kwa makolo athu kudya zipatso zace ndi zokoma zace, taonani, ife ndife akapolo m'menemo.

37. Ndipo licurukitsira mafumu zipatso zace, ndiwo amene munawaika atiweruze, cifukwa ca zoipa zathu; acitanso ufumu pa matupi athu, ndi pa zaweta zathu, monga umo akonda; ndipo ife tisauka kwakukuru.

38. Ndipo mwa ici conse ticita pangano lokhazikika, ndi kulilemba, ndi akulu athu, Alevi athu, ndi ansembe athu, alikomera cizindikilo.

Werengani mutu wathunthu Nehemiya 9