Ndi msonkhano wonse wa iwo oturuka m'ndende anamanga misasa, nakhala m'misasamo; pakuti ciyambire masiku a Yesuwa mwana wa Nuni kufikira tsiku lija ana a Israyeli sanatero. Ndipo panali cimwemwe cacikuru.