Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Nehemiya 7:39-54 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

39. Ansembe: ana a Yedaya, a nyumba ya Yesuwa, mazana asanu ndi anai mphambu makumi asanu ndi awiri kudza atatu.

40. Ana a Imeri, cikwi cimodzi mphambu makumi asanu kudza awiri.

41. Ana a Pasuru, cikwi cimodzi mphambu mazana awiri kudza makumi anai ndi asanu ndi awiri.

42. Ana a Harimu, cikwi cimodzi mphambu khumi limodzi kudza asanu ndi awiri.

43. A Levi: ana a Yesuwa, a Kadimiyeli, a ana a Hodeva, makumi asanu ndi awiri kudza anai.

44. Oyimbira: ana a Asafu, zana limodzi mphambu makumi anai kudza asanu ndi atatu.

45. Odikira: ana a Salumu, ana a Ateri, ana a Talimoni, ana a Akubu, ana a Hatita, ana a Sobai, zana limodzi mphambu makumi atatu kudza asanu ndi atatu.

46. Anetini: ana a Ziha, ana a Hasufa, ana a Tabaoti,

47. ana a Kerosi, ana a Siya, ana a Padoni,

48. ana a Lebana, ana a Hagaba, ana a Salimai,

49. ana a Hanani, ana a Gideri, ana a Gahara,

50. ana a Reaya, ana a Rezini, ana a Nekoda,

51. ana a Gazamu, ana a Uza, ana a Paseya,

52. ana a Besai, ana a Meunimu, ana a Nefusesimu,

53. ana a Bakibuki, ana a Hakufa, ana a Harihuri,

54. ana a Baziliti, ana a Mehida, ana a Harisa,

Werengani mutu wathunthu Nehemiya 7