Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Nehemiya 7:37-45 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

37. Ana a Lodi, Hadidi, ndi Ono, mazana asanu ndi awiri mphambu makumi awiri kudza mmodzi.

38. Ana a Senaa, zikwi zitatu mphambu mazana asanu ndi anai kudza makumi atatu.

39. Ansembe: ana a Yedaya, a nyumba ya Yesuwa, mazana asanu ndi anai mphambu makumi asanu ndi awiri kudza atatu.

40. Ana a Imeri, cikwi cimodzi mphambu makumi asanu kudza awiri.

41. Ana a Pasuru, cikwi cimodzi mphambu mazana awiri kudza makumi anai ndi asanu ndi awiri.

42. Ana a Harimu, cikwi cimodzi mphambu khumi limodzi kudza asanu ndi awiri.

43. A Levi: ana a Yesuwa, a Kadimiyeli, a ana a Hodeva, makumi asanu ndi awiri kudza anai.

44. Oyimbira: ana a Asafu, zana limodzi mphambu makumi anai kudza asanu ndi atatu.

45. Odikira: ana a Salumu, ana a Ateri, ana a Talimoni, ana a Akubu, ana a Hatita, ana a Sobai, zana limodzi mphambu makumi atatu kudza asanu ndi atatu.

Werengani mutu wathunthu Nehemiya 7