Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Nehemiya 6:12-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Ndipo ndinazindikira kuti sanamtuma Mulungu; koma ananena coneneraco pa ine, popeza Tobiya ndi Sanibalati adamlembera.

13. Anamlembera cifukwa ca ici, kuti ine ndicite mantha, ndi kucita cotero, ndi kucimwa; ndi kuti anditolerepo mbiri yoipa ndi kundinyoza.

14. Mukumbukile, Mulungu wanga, Tobiya ndi Sanibalati monga mwa nchito zao izi, ndi Nowadiya mneneri wamkazi yemwe, ndi aneneri otsala, amene anafuna kundiopsa.

15. Ndipo linga linatsirizika pa tsiku la makumi awiri ndi lacisanu la mwezi wa Eluli, titalimanga masiku makumi asanu mphambu awiri.

16. Ndipo kunali atacimva adani athu onse, amitundu onse akutizinga anaopa, nagwadi nkhope; popeza anazindikira kuti nchitoyi inacitika ndi Mulungu wathu.

17. Masikuwo aufulu a Yuda analemberanso akalata ambiri kwa Tobiya; ndipo anawafikanso akalata ace a Tobiya.

18. Pakuti ambiri m'Yuda analumbirirana naye cibwenzi; popeza ndiye mkamwini wace wa Sekaniya mwana wa Ara; ndi mwana wace Yehohanana adadzitengera mwana wamkazi wa Mesulamu mwana wa Berekiya.

19. Anachulanso nchito zace zokoma pamaso panga namfotokozera iye mau anga. Ndipo Tobiya anatumiza akalata kuti andiopse ine.

Werengani mutu wathunthu Nehemiya 6