Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Nehemiya 6:1-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Kunali tsono, atamva Sanibalati, ndi Tobiya, ndi Gesemu M-arabu, ndi adani athu otsala, kuti ndidatha kumanga lingali, posatsalaponso popasuka; (ngakhale pajapo sindinaika zitseko pazipata);

2. anatumiza mau kwa ine Sanibalati ndi Gesemu, kuti, Tiyeni tikomane ku midzi ya ku cigwa ca Ono; koma analingirira za kundicitira coipa.

3. Ndipo ndinawatumizira mithenga, ndi kuti, Ndirikucita nchito yaikuru, sindikhoza kutsika; ndiidulirenji padera nchito poileka ine, ndi kukutsikirani?

4. Nanditumizira ine mau otere kanai; ndinawabwezeranso mau momwemo.

5. Pamenepo Sanibalati anatuma mnyamata wace kwa ine kacisanu, ndi kalata wosatseka m'dzanja mwace;

6. m'menemo mudalembedwa, Kwamveka mwa amitundu, ndi Gasimu acinena, kuti iwe ndi Ayuda mulikulingirira za kupanduka; cifukwa cace mulikumanga lingali; ndipo iwe udzakhala mfumu yao monga mwa mau awa.

Werengani mutu wathunthu Nehemiya 6