Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Nehemiya 5:1-5 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Pamenepo panamveka kulira kwakukuru kwa anthu ndi akazi ao kudandaula pa abale ao Ayuda.

2. Popeza panali ena akuti, Ife, ana athu amuna ndi akazi, ndife ambiri; talandira tirigu, kuti tidye tikhale ndi moyo.

3. Panali enanso akuti, Tirikupereka cikole minda yathu, ndi minda yathu yampesa ndi nyumba zathu; kuti tilandire tirigu cifukwa ca njalayi.

4. Panali enanso akuti, Takongola ndarama za msonkho wa mfumu; taperekapo cikole minda yathu, ndi minda yathu yampesa.

5. Koma tsopano thupi lathu likunga thupi la abale athu, ana athu akunga ana ao; ndipo taonani, titengetsa ana athu amuna ndi akazi akhale akapolo, ndi ana athu akazi ena tawatengetsa kale; ndipo tiribe ife mphamvu ya kucitapo kanthu; ndi minda yathu, ndi minda yathu yampesa, nja ena.

Werengani mutu wathunthu Nehemiya 5