Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Nehemiya 2:1-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Koma kunacitika mwezi wa Nisana, caka ca makumi awiri ca Aritasasta mfumu pokhala vinyo pamaso pace, ndinatenga vinyoyo ndi kuipatsa mfumu. Koma sindidakhala wacisoni pamaso pace ndi kale lonse.

2. Ninena nane mfumu, Nkhope yako nja cisoni cifukwa ninji popeza sudwala? ici si cinthu cina koma cisoni ca mtima. Pamenepo ndinacita mantha akuru.

3. Ndipo ndinati kwa mfumu, Mfumu ikhale ndi moyo kosatha; ilekerenji nkhope yanga kucita cisoni, popeza pali bwinja kumudzi kuli manda a makolo anga, ndi zipata zace zopsereza ndi moto.

4. Ndipo mfumu inati kwa ine, Ufunanji iwe? Pamenepo ndinapemphera Mulungu wa Kumwamba.

5. Ndipo ndinati kwa mfumu, Cikakomera mfumu, ndi mtima wanu ukakomera kapolo wanu, munditumize ku Yuda ku mudzi wa manda a makolo anga, kuti ndiumange.

6. Ninena nane mfumu, irikukhala pansi pamodzi ndi mkazi wace wamkuru, Ulendo wako ngwa nthawi yanji, udzabweranso liti? Ndipo kudakonda mfumu kunditumiza nditaichula nthawi.

7. Ndinanenanso kwa mfumu, Cikakomera mfumu, indipatse akalata kwa ziwanga za tsidya lija la mtsinje, andilole ndipitirire mpaka ndifikira ku Yuda;

Werengani mutu wathunthu Nehemiya 2