Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Nehemiya 13:22-31 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

22. Ndipo ndinauza Alevi kuti adziyeretse, nabwere, nasunge pazipata kupatula dzuwa la Sabata. Mundikumbukire Icinso, Mulungu wanga, ndi kundileka monga mwa cifundo canu cacikuru.

23. Masiku aja ndinaonanso Ayudawo anadzitengera akazi a Asidodi, Aamoni, ndi Amoabu,

24. ndi ana ao analankhula mwina Ciasidodi, osadziwitsa kulankhula Ciyuda, koma monga umo amalankhula mtundu wao uli wonse.

25. Ndipo ndinatsutsana nao, ndi kuwatemberera, ndi kukantha ena a iwo, ndi kumwetula tsitsi lao, ndi kuwalumbiritsa pa Mulungu ndi kuti, Musapereka ana anu akazi kwa ana ao amuna, kapena kutengera ana anu amuna, kapena a inu nokha, ana ao akazi.

26. Nanga Solomo mfumu ya Israyeli sanacimwa nazo zinthu izi? cinkana mwa amitundu ambiri panalibe mfumu ngati iye, ndi Mulungu wace anamkonda, ndi Mulungu wace anamlonga mfumu ya Aisrayeli onse; koma ngakhale iye, akazi acilendo anamcimwitsa.

27. Ndipo kodi tidzamvera inu, kucita coipa ici cacikuru conse, kulakwira Mulungu wathu ndi kudzitengera akazi acilendo?

28. Koma wina wa ana a Yoyada, mwana wa Eliasibu mkuru wa ansembe, anali mkamwini wa Sanibalati Mhoroni; cifukwa cace ndinampitikitsa kumcotsa kwa ine.

29. Muwakumbukile Mulungu wanga, popeza anadetsa unsembe, ndi pangano la unsembe, ndi la Alevi.

30. Momwemo ndinawayeretsa kuwacotsera acilendo onse, ndi kuikira udikiro ansembe ndi Alevi, yense ku nchito yace;

31. ndi copereka ca nkhuni pa nthawi zoikika, ndi wa zipatso zoyamba. Mundikumbukile, Mulungu wanga, cindikomere.

Werengani mutu wathunthu Nehemiya 13