Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Nehemiya 13:2-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. popeza sanawacingamira ana a Israyeli ndi cakudya ndi madzi, koma anawalemberera Balamu awatemberere; koma Mulungu wathu anasanduliza tembererolo likhale mdalitso.

3. Ndipo kunali, atamva cilamuloco, anasiyanitsa pa Israyeli anthu osokonezeka onse.

4. Cinkana ici, Eliasibu wansembe, woikidwa asunge zipinda za nyumba ya Mulungu wathu, anacita cibale ndi Tobiya,

5. namkonzera cipinda cacikuru, kumene adasungira kale zopereka za ufa, libano, ndi zipangizo, ndi limodzi limodzi la magawo khumi a tirigu, vinyo, ndi mafuta, zolamutidwira Alevi, ndi oyimbira, ndi odikira, ndi nsembe zokweza za ansembe.

6. Koma pocitika ici conse sindinakhala ku Yerusalemu; pakuti caka ca makumi atatu ndi caciwiri ca Aritasasta mfumu ya Babulo ndinafika kwa mfumu, ndipo atapita masiku ena ndinapempha mfumu indilole;

7. ndipo ndinafika ku Yerusalemu, ndi kuzindikira coipa anacicita Eliasibu, cifukwa ca Tobiya, ndi kumkonzera cipinda m'mabwalo a nyumba ya Mulungu.

8. Ndipo ndinaipidwa naco kwambiri, motero ndinataya kubwalo akatundu onse a m'nyumba ya Tobiya, kuwacotsa m'cipindamo.

9. Pamenepo ndinalamulira, ndipo anayeretsa zipindazo; ndipo ndinabwezeramonso zipangizo za nyumba ya Mulungu, pamodzi ndi zopereka za ufa ndi libano.

10. Ndinazindikiranso kuti sanapereka kwa Alevi magawo ao; m'mwemo Alevi ndi oyimbira adathawira yense ku munda wace.

11. Potero ndinatsutsana nao olamulira, ndinati, Yasiyidwiranji nyumba ya Mulungu? Ndipo ndinawasonkhanitsa, ndi kuwafka m'malo mwao.

Werengani mutu wathunthu Nehemiya 13