Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Nehemiya 12:26-33 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

26. Awa anakhala m'masiku a Yoyakimu mwana wa Yesuwa, mwana wa Yozadaki, ndi m'masiku a Nehemiya kazembe, ndi a Ezara wansembe mlembiyo.

27. Ndipo popereka linga la Yerusalemu anafunafuna Alevi m'malo mwao monse, kubwera nao ku Yerusalemu, kuti acite kuperekaku mokondwera, ndi mayamiko, ndi kuyimbira, ndi nsanje, zisakasa, ndi azeze.

28. Ana a oyimbirawo anasonkhana ocokera ku dziko lozungulira Yerusalemu, ndi ku midzi ya Anetofati,

29. ndi ku Betegiligala, ndi ku minda ya Geba ndi Azimaveti; popeza oyimbirawo adadzimangira midzi pozungulira Yerusalemu.

30. Ndipo ansembe ndi Alevi anadziyeretsa okha, nayeretsa anthu, ndi zipata, ndi linga.

31. Pamenepo ndinakwera nao akuru a Yuda pa lingali, ndinaikanso oyamikira magulu awiri akuru oyenda molongosoka; lina loyenda ku dzanja lamanja palinga kumka ku cipata ca kudzala;

32. ndi pambuyo pao anayenda Hosaya, ndi limodzi la magawo awiri a akuru a Yuda,

33. ndi Azariya, Ezara ndi Mesulamu,

Werengani mutu wathunthu Nehemiya 12