Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Nehemiya 12:21-26 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

21. wa Hilikiya, Hasabiya; wa Yedaya, Netaneli.

22. M'masiku a Ehasibi, Yoyada, Yohanana, ndi Yoduwa, Alevi analembedwa akuru a nyumba za makolo; ansembe omwe, mpaka ufumu wa Dariyo wa ku Perisiya.

23. Ana a Levi, akuru a nyumba za makolo, analembedwa m'buku la macitidwe, mpaka masiku a Yohanana mwana wa Eliasibu.

24. Ndi akuru a Alevi: Hasabiya, Serebiya, ndi Yesuwa mwana wa Kadimiyeli, ndi abale ao openyana nao, kulemekeza ndi kuyamika, monga mwa lamulo la Davide munthu wa Mulungu, alonda kupenyana alonda.

25. Mataniya, ndi Bakibukiya, Obadiya, Mesulamu, Talimoni, Akubi, ndiwo odikira akulonda pa nyumba za cuma ziri kuzipata.

26. Awa anakhala m'masiku a Yoyakimu mwana wa Yesuwa, mwana wa Yozadaki, ndi m'masiku a Nehemiya kazembe, ndi a Ezara wansembe mlembiyo.

Werengani mutu wathunthu Nehemiya 12