Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Nehemiya 11:8-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Ndi wotsatananaye Gabai, Salai, mazana asanu ndi anai mphambu makumi awiri kudza asanu ndi atatu.

9. Ndi Yoeli mwana wa Zikiri ndiye woyang'anira wao, ndi Yuda mwana wa Hasenuwa ndiye wothandizana naye, poyang'anira mudzi.

10. Mwa ansembe: Yedaya mwana wa Yoyaribi, Yakini,

11. Seraya mwana wa Hilikiya, mwana wa Mesulamu, mwana wa Zadoki, mwana wa Merayoti, mwana wa Ahitubu mtsogoleri wa m'nyumba ya Mulungu;

12. ndi abale ao ocita nchito ya m'nyumbayi ndiwo mazana asanu ndi atatu mphambu makumi awiri kudza awiri; ndi Adaya mwana wa Yerohamu, mwana wa Pelaliya, mwana wa Amzi, mwana wa Zekariya, mwana: wa Pasuru, mwana wa Malikiya;

13. ndi abale ace akulu a nyumba za makolo awiri mphambu makumi anai kudza awiri, ndi Amasai mwana wa Azareli, mwana wa Azai, mwana wa Mesilimoti, mwana wa Imeri;

14. ndi abale ao, ngwazi zamphamvu, zana limodzi mphambu makumi awiri kudza asanu ndi atatu; ndi woyang'anira wao ndiye Zabidiyeli mwana wa Hagedolimu.

Werengani mutu wathunthu Nehemiya 11