Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Nehemiya 11:22-29 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

22. Ndipo woyang'anira wa Alevi m'Yerusalemu ndiye Uzi mwana wa Bani, mwana wa Hasabiya, mwana wa Mataniya, mwana wa Mika; mwa ana a Asafu oyimbira ena anayang'anira nchito ya m'nyumba ya Mulungu.

23. Pakuti mfumu inalamulira za iwowa, naikira oyimbira cowathandiza, yense cace pa tsiku lace.

24. Ndi Petatiya mwana wa Mesezabele, wa ana a Zera, mwana wa Yuda, anatumikira mfumu pa mirandu yonse ya anthuwo.

25. Ndi ana ena a Yuda anakhala m'midzi ya ku minda yao, m'Kiriyati Ariba ndi miraga yace, ndi m'Diboni ndi miraga yace, ndi m'Yekabizeeli ndi midzi yace,

26. ndi m'Yesuwa, ndi m'Molada, ndi Betepeleti,

27. ndi m'Hazarisuala, ndi m'Beereseba ndi miraga yace,

28. ndi m'Zikilaga, ndi m'Mekona ndi miraga yace,

29. ndi m'Enirimoni, ndi m'Zora, ndi m'Yarimuti,

Werengani mutu wathunthu Nehemiya 11