Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Nehemiya 11:19-24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

19. Ndi odikira: Akubu, Talimoni, ndi abale ao akulindira pazipata, ndiwo zana limodzi mphambu makumi asanu ndi awiri kudza awiri.

20. Ndi Aisrayeli otsala, ndiwo ansembe ndi Alevi, anakhala m'midzi yonse ya Yuda, yense m'colowa cace.

21. Koma Anetini anakhala m'Ofeli, ndi Ziya, ndi Gisipa anali oyang'anira Anetini.

22. Ndipo woyang'anira wa Alevi m'Yerusalemu ndiye Uzi mwana wa Bani, mwana wa Hasabiya, mwana wa Mataniya, mwana wa Mika; mwa ana a Asafu oyimbira ena anayang'anira nchito ya m'nyumba ya Mulungu.

23. Pakuti mfumu inalamulira za iwowa, naikira oyimbira cowathandiza, yense cace pa tsiku lace.

24. Ndi Petatiya mwana wa Mesezabele, wa ana a Zera, mwana wa Yuda, anatumikira mfumu pa mirandu yonse ya anthuwo.

Werengani mutu wathunthu Nehemiya 11