Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Nehemiya 11:14-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. ndi abale ao, ngwazi zamphamvu, zana limodzi mphambu makumi awiri kudza asanu ndi atatu; ndi woyang'anira wao ndiye Zabidiyeli mwana wa Hagedolimu.

15. Ndi mwa Alevi: Semaya mwana wa Hasubu, mwana wa Azirikamu, mwana wa Hasabiya, mwana wa Buni;

16. ndi Sabetai, ndi Yozabadi, mwa akuru a Alevi, anayang'anira nchito za pabwalo za nyumba ya Mulungu;

17. ndi Mataniya mwana wa Mika, mwana wa Zabidi, mwana wa Asafu, ndiye mkuru wakuyamba mayamiko, popemphera; ndi Bakibukiya wotsatana naye mwa abale ace, ndi Abida mwana wa Samua, mwana wa Galali, mwana wa Yedutuni.

18. Alevi onse m'mudzi wopatulikawo ndiwo mazana awiri mphambu makumi asanu ndi atatu kudza anai.

19. Ndi odikira: Akubu, Talimoni, ndi abale ao akulindira pazipata, ndiwo zana limodzi mphambu makumi asanu ndi awiri kudza awiri.

Werengani mutu wathunthu Nehemiya 11