Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Nehemiya 11:1-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo akuru anthu anakhala m'Yerusalemu; anthu otsala omwe anacita maere, kuti libwere limodzi la magawo khumi likhale m'Yerusalemu, mudzi wopatulika, ndi asanu ndi anai a khumi m'midzi yina.

2. Ndipo anthu anadalitsa amuna onse a akudzinenera mwaufulu kuti adzakhala m'Yerusalemu.

3. Awa tsono ndi akulu a dziko okhala m'Yerusalemu; koma m'midzi ya Yuda yense anakhala pa colowa cace m'midzi mwao, ndiwo Israyeli, ansembe, ndi Alevi, ndi Anetini, ndi ana a akapolo a Solomo.

4. Ndipo m'Yerusalemu munakhala ena a ana a Yuda ndi a ana a Benjamini. Mwa ana a Yuda: Ataya mwana wa Uziya, mwana wa Zekariya, mwana wa Amariya, mwana wa Sefatiya, mwana wa Mahalaleli, wa ana a Perezi;

5. ndi Maaseya mwana wa Baruki, mwana wa Koloze, mwana wa Huzaya, mwana wa Adaya, mwana wa Yoyaribi, mwana wa Zekariya, mwana wa Msiloni.

6. Ana onse a Perezi okhala m'Yerusalemu ndiwo ngwazi mazana anai mphambu makumi asanu ndi limodzi kudza asanu ndi atatu.

7. Ndi ana a Benjamini ndi awa: Salu mwana wa Mesulamu, mwana wa Yoedi, mwana wa Pedaya, mwana Wa Kolaya, mwana wa Maseya, mwana wa Itiyeli, mwana wa Yesaya.

8. Ndi wotsatananaye Gabai, Salai, mazana asanu ndi anai mphambu makumi awiri kudza asanu ndi atatu.

9. Ndi Yoeli mwana wa Zikiri ndiye woyang'anira wao, ndi Yuda mwana wa Hasenuwa ndiye wothandizana naye, poyang'anira mudzi.

Werengani mutu wathunthu Nehemiya 11