Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Nehemiya 1:1-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. MAU a Nehemiya mwana wa Hakaliya. Kunali tsono mwezi wa Kisilevi, caka ca makumi awiri, pokhala ine ku Susani ku nyumba ya mfumu,

2. anafika Hanani, mmodzi wa abale anga, iye ndi amuna ena a ku Yuda; ndipo ndinawafunsa za Ayuda adapulumukawo otsala andende, ndi za Yerusalemu.

3. Nanena nane iwo, Otsalawo otsala andende uko ku dzikoko akulukutika kwakukuru, nanyozedwa; ndi linga la Yerusalemu lapasuka, ndi zipata zace zatenthedwa ndi moto.

4. Ndipo kunali, pakumva'mau awa, ndinakhala pansi ndi kulira misozi, ndi kucita maliro masiku ena, ndinasalanso, ndi kupemphera pamaso pa Mulungu wa Kumwamba,

5. ndi kuti, Ndikupembedzani Yehova, Mulungu wa Kumwamba, Mulungu wamkuru ndi woopsa, wakusunga pangano ndi cifundo ndi iwo akumkonda ndi kusunga malamulo ace;

6. muchere khutu, ndi maso anu atseguke kumvera pemphero la kapolo wanu, ndilipempha pamaso panu tsopano apa msana ndi usiku, kupempherera ana a Israyeli akapolo anu, ndi kuulula zoipa za ana a Israyeli zimene tacimwira nazo Inu; inde tacimwa, ine ndi nyumba ya atate wanga.

7. Tacita mwamphulupulu pa Inu, osasunga malamulo, kapena malemba, kapena maweruzo, amene mudalamulita mtumiki wanu Mose.

Werengani mutu wathunthu Nehemiya 1